WOCHOTSA MASAUTSO (#13491)

55.	O Inu amene mayesero Ake ndi mankhwala ochiritsa kwa iwo amene ali pafupi Nanu, lupanga Lake liri chifuniro chopambana cha onse amene akukondani Inu, mubvi Wake ndi pempho lapamtima la mitima ya iwo amene akuzindikira choonadi Chanu! Ndikupemphani, mwa kukoma Kwanu kwa uzimu ndi kunyezimira kwa ulemelero wa nkhope Yanu, kuti Mutitumizire ife kuchokera ku malo Anu m’mwamba chimene chingatipangitse ife kuyandikira kwa Inu.  
Choncho Limbikitsani mapazi athu, O Mulungu wanga M’Chiphunzitso Chanu, ndipo Walitsani mitima yathu ndi kuwala kwa nzeru Zanu, ndipo Unikirani m’zifuwa zathu ndi kuunika kwa Maina Anu.

-Bahá'u'lláh
-----------------------

WOCHOTSA MASAUTSO (#13489)

Kodi palinso wina Wochotsa masautso kupatula Mulungu? Nenani: Atamandike Mulungu! Iye Ndiye Mulungu! Onse ndi antchito Ake ndipo onse akhala mu ulamuliro Wake!

-The Báb
-----------------------

WOCHOTSA MASAUTSO (#13490)

54.	Tinene: Mulungu Akwaniritsa zinthu zonse pamwamba pa zinthu zonse, ndipo kulibe chilichonse kumwamba kapena m’dziko lapansi koma Mulungu Akwaniritsa. Indetu, Iye Ali mwa Iye Mwini Wodziwa, Wosasowakathu, Mwinimphamvu.

-The Báb
-----------------------

WOCHOTSA MASAUTSO (#13492)

Iye ndi Wachisoni, Wachaulere Chonse! O Mulungu, 
Mulungu wanga! Inu mukundiwona ine, Inu mukundidziwa ine; Inu amene muli Panthunzi panga ndi 
Pothawira panga, Palibe amene ndasankha kapena kufufuza kupatula Inu, palibe njira yomwe ine ndayendamo kapena kufuna kudzayenda koma mnjira Yanu ya chikondi Chanu.  
Mu mdima wa ndiwe yani wa mabvuto, maso anga amatembenukira ndi oyembekezo ndi odzadzidwa ndi chikhulupiriro ku m'mawa wa chifundo Chanu chopanda malire ndipo ora la m’bandakucha mzimu wanga wofoka umatsitsitmutsidwa ndi kulimbikitsidwa pokumbukira kukongola Kwanu ndi ungwiro Wanu. Iye amene chisomo cha chifundo Chake chamuthandiza, ngakhale kuti katakhala kadontho kakang’ono, kadzasanduka nyanja yopanda malire, ndipo kanthu kochepetsetsa kamene kathandizidwa ndi chifundo Chake, kadzawala ngati nyenyezi lowalitsitsa.”  
“Khalani pansi pa chitetezo Changa, O Mzimu Wanga wa chiyero, Inu amene muli Opereka Zaulere Zonse, wantchito Wanu uyu wokondedwa ndi, wowalitsidwa. Muthandizeni mu dziko ili la umunthu kuti akhale osagwedezeka ndi olimba mu chikondi Chanu ndipo mpatseni iye amene ali mbalame yothyoka phiko kuti apeze pothawira ndi mthuzi wa chisa Chanu cha uzimu chimene chakhazikika pa mtengo wa kumwamba.”

-`Abdu'l-Bahá
-----------------------

